• Privacy & Policy
Sunday, July 27, 2025
The Pangolin
  • Home
  • News
  • Special Report
  • National
  • Opinion
  • Che Chitekwe
  • Business
  • Entertainment
  • Sports
No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Special Report
  • National
  • Opinion
  • Che Chitekwe
  • Business
  • Entertainment
  • Sports
No Result
View All Result
The Pangolin
No Result
View All Result
Home Featured Stories

Mphuzitsi wa pa M’ngwangwa wavomereza kuti anawalembera mayeso a Gangata

Grace Imran by Grace Imran
May 13, 2025
in Featured Stories, Editor’s Pick, National, News, Special Report
Reading Time: 2 mins read
Mphuzitsi wa pa M’ngwangwa wavomereza kuti anawalembera mayeso a Gangata
0
SHARES
21
VIEWS

Mmodzi mwa mboni zaboma pamulandu omwe wachiwiri kwa  mtsogoleri wa chipani cha Democratic Progressive Party (DPP) mchigawo cha pakati, a Alfred Gangata, akuwaganizira kuti adapeza setifiketi ya MSCE  mwachinyengo, wavomeleza kuti iye ndi amene anamulembera Mayeso mkuluyu.

 A Andrew Elia Mphamba, omwe ndi mphunzitsi pasukulu ya sekondale ya M’ngwangwa, avomereza izi pamene akupereka umboni m’bwalo la milandu mu mzinda wa Lilongwe.

Iwo avomera kuti akuwadziwa a Gangata ndipo ati muchaka cha 2017, anaimbiridwa lamya ndi wachiwiri wa mtsogoleri wa DPPyu kuti akumane ku City Centre ku Lilongwe.

Atakumana, iwo ati anawawuza kuti apite kunyumba kwawo ku Area 9 ku Lilongwe komwe anakawauza kuti akufuna thandizo lawo kuti awalembere mayeso ndipo kuti awapatsa K4 million komanso galimoto, mwazina.

Iwo ati anavomera kutero ndipo a Gangata anawapatsa zoyenerera monga ndalama kuti apeze sukulu yokalembera mayeso komanso kuti achite dongosolo lonse lamayeso mpaka atamaliza mayeso awo.

A Mphamba ati anapeza sukulu ya sekondale ya Chitowo yomwe ili ku Dedza kuti akalembe mayesowo ndipo anagwiritsa ntchito dzina la Alfred Gangata ngati dzina lawo lolembera mayeso.

Mayeso a 2018 atatuluka, mboniyi yati anayenda bwino ndipo anakhoza. Iwo ati anali osangalala kuti apeza ndalama pokumbukira lonjezo landalama ndi zina zomwe analonjezana ndi a Gangata.

Mboniyi yati nthawi itakwana yoti awapatse ndalama komanso zinthu zomwe anawalonjeza, a Gangata amachedwa kupeleka ndipo anawauza kuti akakatenga certificate zonse awapatsa.

Atakatenga certificate, mboniyi yati anapita ku ofesi kwa a Gangata kuti akasiye ndipo atayisiya anawauza kuti apiteso tsiku lina kukatenga zomwe anawalonjeza.

Atapita anawauza kuti ndalama pakanalibe ndipo mboniyi yati pakhala thawi akulimbana kuti awapatse zomwe anawalonjeza.

A Mphamba anauza bwaloli kuti kufikira pano palibe zomwe iwo anapezako kapena kulandira kuchokera kwa a Gangata, malinga ndi zomwe analonjezana kuti awalembere mayeso.

Pano, tsopano bwaloli lawonetsa certificate kwamboniyi ndipo mboniyi yavomera kuti ndiyomweyidi yomwe iwo analembera mayeso mmalo mwa a Gangata.

Bwaloli lauza mboniyi kuti ifotokoze kuti zikutheka bwanji kuti iwo analembera mayeso a Gangata pogwiritsa ntchito Chithunzi cha a Gangata.

A Mpamba ati anachita zotheka kuti zitheke motero.

Mboniyi yatiso ngakhale mphunzitsi wamkulu komanso wachiwiri pasukulu ya sekondale ya Chitowo, komwe iwo analembera mayesowo, atha kuwazindikira ndidzina loti Alfred Gangata.

Kufikira apa, bwaloli layamba laima kaye kumva mlanduwu ndipo lati lidzapitiriza pa 27 May chaka chino.

Woyimira a Gangata pa mulanduwu a Khwima Mchizi ati ali wokonzeka kufunsa mafunso a Mphamba mulanduwu ukadzabweranso m’bwaloli.

ShareSendTweetSendShareShare

Recent News

The DPP’s Desperate Charade at BICC Exposes a Party in Denial and Afraid to Face the Naked Truth

The Cruel Captivity of Arthur Peter Mutharika

July 26, 2025
75
The Return of the Cashgate Duo

The Return of the Cashgate Duo

July 26, 2025
62
Mtambo Breaks Ranks with Chihana says He Will Not Campaign for DPP

Mtambo Breaks Ranks with Chihana says He Will Not Campaign for DPP

July 25, 2025
197
The DPP’s Desperate Charade at BICC Exposes a Party in Denial and Afraid to Face the Naked Truth

The DPP’s Desperate Charade at BICC Exposes a Party in Denial and Afraid to Face the Naked Truth

July 25, 2025
130
  • Privacy & Policy

© 2025 The Pangolin - All Rights Reserved.

Welcome Back!

Login to your account below

Forgotten Password?

Retrieve your password

Please enter your username or email address to reset your password.

Log In

Add New Playlist

No Result
View All Result
  • Home
  • News
  • Special Report
  • National
  • Opinion
  • Che Chitekwe
  • Business
  • Entertainment
  • Sports

© 2025 The Pangolin - All Rights Reserved.

-
00:00
00:00

Queue

Update Required Flash plugin
-
00:00
00:00